Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 45:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Zitamveka kunyumba kwa Farao kuti abale a Yosefe abwera, Faraoyo ndi antchito ake onse adakondwa kwambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Akunyumba kwa Farao atamva kuti abale ake a Yosefe abwera, Farao pamodzi ndi nduna zake zonse anakondwera.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 45:16
15 Mawu Ofanana  

Koma Abramu anati kwa Sarai, Taona, mdzakazi wako ali m'dzanja lako, umchitire iye chimene chikukomera m'maso mwako. Ndipo Sarai anamsautsa iye, ndipo anathawa kumaso kwake.


Ndipo Abimeleki anati, Taona dziko langa lili pamaso pako; kumene kuli kwabwino pamaso pako takhala kumeneko.


Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori.


Tsopano, Farao afunefune munthu wakuzindikira ndi wanzeru, amkhazike iye ayang'anire dziko la Ejipito.


Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake.


Ndipo anampsompsona abale ake onse, nalirira iwo; ndipo pambuyo pake abale ake onse anacheza naye.


Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Nena ndi abale ako, Chitani ichi; senzetsani nyama zanu, ndi kupita kunka ku dziko la Kanani;


Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.


Ndipo chinthuchi chinayenera m'maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.


Ndipo mauwo anakonda mfumu ndi akalonga; ndi mfumu inachita monga mwa mau a Memukana,


ndi namwali womkonda mfumu akhale mkazi wamkulu m'malo mwa Vasiti. Ndipo chinthuchi chinamkonda mfumu, nachita chomwecho.


Pamenepo Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse ananena naye, Apange mtengo, msinkhu wake mikono makumi asanu, ndi mawa mukanene nayo mfumu kuti ampachike Mordekai pamenepo; nimulowe pamodzi ndi mfumu kumadyerero wokondwera. Ndipo ichi chidakomera Hamani, napangitsa anthu mtengowo.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.


amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa