Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 44:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Yosefe anauza tsanyumba wake kuti, Dzaza matumba a anthuwo ndi chakudya, monga angathe kunyamula, ndi kuika ndalama za yense kukamwa kwa thumba lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake Yosefe adalamula wantchito wamkulu woyang'anira nyumba yake kuti, “Dzaza matumba a anthuŵa ndi chakudya chambiri momwe angathe kusenzera. Ndipo ndalama za aliyense uziike pakamwa pa thumba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 44:1
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati kwa mnyamata wake wamkulu wa pa nyumba yake, amene analamulira pa zonse anali nazo, Taikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga:


Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.


Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.


Ndipo pamene Yosefe anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wake, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakonzere, chifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.


Ndipo anayandikira kwa tsanyumba wa Yosefe, ndipo ananena ndi iye pa khomo la nyumba, nati,


Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Ejipito atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife chakudya pang'ono.


Nuike chikho changa, chikho chasiliva chija, kukamwa kwa thumba la wamng'ono, pamodzi ndi ndalama za tirigu zake. Ndipo iye anachita monga mau ananena Yosefe.


Ndipo onani, Ambuye, Yehova wa makamu, wachotsa ku Yerusalemu ndi ku Yuda mchirikizo wochirikiza chakudya chonse ndi madzi onse, zimene zinali mchirikizo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa