Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 43:12 - Buku Lopatulika

12 nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanachite dala;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Mutenge ndalama zokwanira, kuti mukabweze ndalama zomwe zidapezeka m'matumba mwanu zija. Makamaka zinthu zinali zitalakwika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Mutenge ndalama zokwanira. Ndalama zina nʼzokamubwezera zija anakuyikirani mʼmatumba anu zija. Mwina anangolakwitsa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 43:12
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe analamulira kuti adzaze zotengera zao ndi tirigu, ndi kubweza ndalama zao, aliyense m'thumba mwake, ndi kuwapatsa phoso la panjira; ndipo anatero nao.


Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lake; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa.


mutengenso mphwanu, nimunyamuke, mupitenso kwa munthu uja:


ndipo panali pamene ife tinafika pachigono, tinamasula matumba athu, ndipo taonani ndalama za yense zinali kukamwa kwa thumba lake, ndalama zathu mkulemera kwake; ndipo tabwera nazo m'manja mwathu.


Ndalama zina tatenga m'manja mwathu kuti tigule chakudya: sitimdziwa amene anaika ndalama zathu m'matumba athu.


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.


pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.


Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.


asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.


Yesani zonse; sungani chokomacho,


Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa