Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:37 - Buku Lopatulika

37 Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

37 Ndipo chinthucho chinali chabwino m'maso mwa Farao, ndi m'maso mwa anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

37 Farao pamodzi ndi nduna zake adavomereza zonse zimene adaanena Yosefe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

37 Farao ndi nduna zake anagwirizana nawo malangizo a Yosefe.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:37
10 Mawu Ofanana  

Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.


Ndipo Farao anati kwa anyamata ake, Kodi ife tidzaone munthu ngati uyu, mzimu wa Mulungu uli m'mtima mwake?


Ndipo mbiri yake inamveka m'nyumba ya Farao, kuti abale ake a Yosefe afika; ndipo inamkomera Farao, ndi anyamata ake.


Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse.


Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake.


kufikira nyengo yakuchitika maneno ake; mau a Yehova anamuyesa.


Lilime la wolungama likunga siliva wosankhika; koma mtima wa oipa uli wachabe.


Mau oyenera a pa nthawi yake akunga zipatso zagolide m'nsengwa zasiliva.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


Pamene Finehasi wansembe, ndi akalonga a msonkhano ndi akulu a mabanja a Israele okhala naye anamva mau adawanena ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, anawakomera pamaso pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa