Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 34:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Sekemu ankamukondadi Dina, mwana wa Yakobe, ndipo ankamulankhula mau achikondi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma Sekemu anamukondadi namwali uja, Dina, mwana wa Yakobo motero kuti anamuyankhula mawu womutonthoza.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:3
11 Mawu Ofanana  

Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.


Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.


Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.


Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.


Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.


Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.


Chifukwa chake taonani, ndidzamkopa ndi kunka naye kuchipululu, ndi kulankhula naye momkonda mtima.


Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzanditcha Mwamuna wanga, osanditchanso Baala wanga.


Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye.


Nakweza iwo mau ao, naliranso misozi; ndi Oripa anampsompsona mpongozi wake, koma Rute anamkangamira.


Ndipo kunali, pakutsiriza iye kulankhula ndi Saulo, mtima wa Yonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Yonatani anamkonda iye monga moyo wa iye yekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa