Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 34:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo ana ake aamuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo ana ake amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma ana a Yakobe adayankha Sekemu ndi bambo wake Hamori moŵanyenga, popeza kuti Sekemu adaamchititsa manyazi Dina mlongo wao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi abambo ake, Hamori mwachinyengo chifukwa mlongo wawo, Dina anali atayipitsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 34:13
17 Mawu Ofanana  

Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.


nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.


Koma inu ndinu opanga zabodza, asing'anga opanda pake inu nonse.


Kodi munenera Mulungu mosalungama, ndi kumnenera Iye monyenga?


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.


ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu; kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga otuluka mumtima.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


nati, Kazinenani, kuti ophunzira ake anadza usiku, namuba Uja m'mene ife tinali m'tulo.


Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi ino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa