Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 31:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo iye anatenga abale ake pamodzi naye, namlondola iye ulendo wa masiku asanu ndi awiri: nampeza iye paphiri la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Tsono adatenga anthu ake, nkulondola Yakobeyo masiku asanu ndi aŵiri, mpaka adakampezera ku dziko lamapiri la Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Pomwepo anatengana ndi abale ake namulondola Yakobo kwa masiku asanu ndi awiri ndipo anakamupezera ku Giliyadi, dziko la mapiri.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 31:23
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anati kwa Loti, Tisachite ndeu, ine ndi iwe, abusa anga ndi abusa ako: chifukwa kuti ife ndife abale.


Ndipo anati, Ayamikike Yehova Mulungu wa Ambuyanga Abrahamu amene sanasiye mbuyanga wopanda chifundo chake ndi zoona zake: koma ine Yehova wanditsogolera m'njira ya kunyumba ya abale ake a mbuyanga.


Tsiku lachitatu anamuuza Labani kuti Yakobo wathawa.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.


M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikumenyana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa