Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 30:26 - Buku Lopatulika

26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Undipatse ine akazi anga ndi ana anga chifukwa cha iwowa ndakutumikira iwe, ndimuke: chifukwa udziwa iwe ntchito imene ndinakugwirira iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Patseni akazi anga ndakugwirirani ntchitoŵa, pamodzi ndi ana anga, ndipo ndichoke. Mukudziŵa kuti ndakugwirirani bwino ntchito.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Patseni akazi anga ndi ana anga, amene ndinakugwirirani ntchito, ndipo ndidzanyamuka ulendo. Inu mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:26
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anamkonda Rakele, nati, Ndidzakutumikirani inu zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele mwana wanu wamkazi wamng'ono.


Ndipo Yakobo analowanso kwa Rakele, namkondanso Rakele kopambana Leya, namtumikira Labani zaka zisanu ndi ziwiri zinanso.


Ndipo Labani anati kwa Yakobo, Wachitanji? Wathawa kwa ine mobisika ndi kutenga ana anga aakazi, monga mikoli ya lupanga.


Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Chifukwa ndinaopa: chifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako aakazi.


Ndipo inu mudziwa kuti ndi mphamvu zanga zonse ndatumikira atate wanu.


Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa