Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 27:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Apo Isaki adafunsa kuti, “Kodi nyama imeneyi waipeza bwanji msanga chotere, mwana wanga?” Yakobe adayankha kuti, “Chauta, Mulungu wanu, adandithandiza kuti ndiipeze.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?” Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 27:20
4 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu mundiyendetse ine bwino lero lino, mumchitire ufulu mbuyanga Abrahamu.


Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.


Kodi munenera Mulungu mosalungama, ndi kumnenera Iye monyenga?


Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa