Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 26:29 - Buku Lopatulika

29 kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudze iwe, sitidakuchitire kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 kuti usatichitire ife zoipa, pakuti sitidakhudza iwe, sitidakuchitira kanthu koma kabwino ndiko, ndipo takulola umuke ndi mtendere; ndiwe tsopano wodalitsidwa ndi Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 kuti simudzatichita zoipa, monga ife sitidakuchiteni zoipa. Tidakuchitirani zabwino, ndipo tidakulolani kuti mupite mwamtendere. Tsopano Chauta wakudalitsani.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 kuti inu simudzatichitira zoyipa monga ifenso sitinakuchitireni nkhondo. Ife tinakuchitirani zabwino zokhazokha, ndipo tinakulolani kuti musamuke kuchoka kwathu mu mtendere. Tsopano Yehova wakudalitsani.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 26:29
8 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako; nukhale iwe mdalitso;


ndipo ndidzadalitsa amene akudalitsa iwe; ndi kutemberera iye amene akutemberera iwe; ndipo mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.


Ndipo panali nthawi yomweyo, Abimeleki ndi Fikolo kazembe wa nkhondo yake anati kwa Abrahamu, kuti, Mulungu ali pamodzi ndi iwe m'zonse uzichita iwe;


kudalitsa ndidzakudalitsa iwe, kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, monga mchenga wa m'mphepete mwa nyanja; ndipo mbeu zako zidzagonjetsa chipata cha adani ao;


Ndipo anati, Talowa iwe, wodalitsidwa ndi Yehova; uimiriranji kunjako? Chifukwa kuti ndakonzeratu nyumba, ndi malo a ngamira.


Odalitsika inu a kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa