Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:65 - Buku Lopatulika

65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

65 Ndipo anati kwa mnyamata, Munthuyo ndani amene ayenda m'munda kukomana ndi ife? Mnyamatayo ndipo anati, Uyo ndi mbuyanga: chifukwa chake namwali anatenga chophimba chake nadziphimba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

65 nafunsa wantchitoyo kuti, “Nanga munthu ali akudza kunoyu ndani?” Wantchito uja adayankha kuti, “Ndiye mbuyanga uja ameneyu.” Motero Rebeka adatenga nsalu, nadziphimba kumaso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

65 nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?” Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:65
9 Mawu Ofanana  

Kwa Sara ndipo anati, Taona, ndapatsa mlongo wako ndalama zasiliva mazana khumi; taona, izo ndizo zoyeretsa maso za kwa onse amene ali ndi iwe: ndi pamaso pa onse ukhale wolungama.


Ndipo Rebeka anatukula maso ake, ndipo pamene anaona Isaki anatsika pa ngamira.


Mnyamatayo ndipo anamuuza Isaki zonse anazichita.


Pamenepo anavula zovala zake zamasiye, nadzifunda ndi chofunda chake, navala nakhala pa chipata cha Enaimu, chifukwa chili panjira ya ku Timna; pakuti anaona kuti Sela anakula msinkhu, ndipo sanampatse iye kuti akhale mkazi wake.


akalirole, ndi nsalu zabafuta, ndi nduwira, ndi zophimba.


Tenga mipero, nupere ufa; chotsa chophimba chako, vula chofunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.


koma mkazi chifukwa cha mwamuna; chifukwa cha ichi mkazi ayenera kukhala nao ulamuliro pamutu pake, chifukwa cha angelo.


Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa