Genesis 24:40 - Buku Lopatulika40 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201440 Ndipo anati kwa ine, Yehova, amene ndiyenda ine pamaso pake, adzatumiza mthenga wake pamodzi ndi iwe, nadzakuyendetsa bwino m'njira yako; ndipo ukamtengere mwana wanga mkazi wa mwa abale anga ndi kunyumba ya atate wanga; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa40 Iye adandiyankha kuti, ‘Chauta amene ndakhala ndikumumvera nthaŵi zonse, adzatuma mngelo wake kuti apite pamodzi nawe, ndipo adzakuthandiza. Udzampezera mkazi mwana wanga pakati pa anthu anga, m'banja la bambo wanga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero40 “Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa. Onani mutuwo |