Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 24:32 - Buku Lopatulika

32 Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Munthuyo ndipo analowa m'nyumba, namasula ngamira, napatsa ngamira udzu ndi chakudya, ndi madzi akusamba mapazi ake ndi mapazi a iwo amene anali naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Motero munthu uja adakaloŵa m'nyumba, ndipo Labani adamasula katundu amene zidaasenza ngamirazo. Atatero adazipatsa chakudya, naŵapatsa madzi alendo onsewo kuti asambe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 24:32
10 Mawu Ofanana  

nditengetu madzi pang'ono, ndikusambitseni mapazi anu, mupumule pansi pa mtengo;


Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.


Ndipo anaika chakudya pamaso pake: koma anati, Sindidzadya ndisananene chimene ndadzera. Ndipo anati, Nenatu.


Ndipo panali pamene Labani anamva mbiri ya Yakobo mwana wa mlongo wake, iye anathamangira kukakomana naye namfungatira, nampsompsona, namlowetsa m'nyumba mwake. Ndipo iye anamfotokozera Labani zinthu zonsezo.


Ndipo munthuyo analowetsa anthu m'nyumba ya Yosefe, nawapatsa iwo madzi, natsuka mapazi ao, napatsa abulu ao chakudya.


Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Pamenepo anamlonga m'nyumba yake, napatsa abulu chakudya; ndipo iwo anasamba mapazi ao, nadya, namwa.


Ndipo iye ananyamuka, nawerama nkhope yake pansi, nati, Onani, mdzakazi wanu ali kapolo wakusambitsa mapazi a anyamata a mbuye wanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa