Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 23:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo ana a Hiti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga lili m'menemo, likhale lake lamanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Motero mundawo pamodzi ndi manda omwewo amene kale adaali a Ahiti, malo onsewo adapatsidwa kwa Abrahamu, ndipo iye adaŵasandutsa manda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Choncho Ahiti anapereka munda pamodzi ndi phanga la mʼmenemo kwa Abrahamu kuti akhale manda.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 23:20
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Kanani anabala Sidoni woyamba wake, ndi Heti,


Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wake m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamure (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.


Ine ndine mlendo wakukhala ndi inu: mundipatse ndikhale ndi manda pamodzi ndi inu, kuti ndiike wakufa wanga ndisamthirenso maso.


munda umene anagula Abrahamu kwa ana a Hiti. Pamenepo anamuika Abrahamu ndi Sara mkazi wake.


Ndipo ana ake Isaki ndi Ismaele anamuika iye m'phanga la Makipela, m'munda wa Efuroni mwana wake wa Zohari Muhiti, umene uli patsogolo pa Mamure;


Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanitsidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,


chifukwa kuti ana ake aamuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.


Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.


Koma mfumu inati kwa Arauna, Iai; koma ndidzaligula kwa iwe pa mtengo wake, pakuti sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe zopsereza zopanda mtengo wake. Momwemo Davide anagula dwalelo ndi ng'ombezo naperekapo masekeli makumi asanu a siliva.


Nagona Manase ndi makolo ake, naikidwa m'munda wa nyumba yake, m'munda wa Uza, nakhala mfumu m'malo mwake Amoni mwana wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa