Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 22:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye paguwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anafika kumalo komwe Mulungu anamuuza iye; ndipo Abrahamu anamanga guwa la nsembe nakonza nkhuni, namanga Isaki mwana wake, namuika iye pa guwa la nsembe pamwamba pa nkhuni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Atafika ku malo amene adaamuuza Mulungu aja, Abrahamu adamanga guwa, naika nkhuni pamwamba pa guwalo. Kenaka adamanga mwana wake uja, namgoneka pamwamba pa nkhunizo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 22:9
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anaonekera kwa Abramu nati, Ndidzapatsa mbeu yako dziko lino: pamenepo anammangira Yehova guwa la nsembe amene anamuonekera iye.


Ndipo iye anachoka kumeneko kunka kuphiri la kum'mawa kwa Betele, namanga hema wake; Betele anali kumadzulo, ndi Ai anali kum'mawa: kumeneko ndipo anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.


Ndipo Abramu anasuntha hema wake nafika nakhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure, imene ili mu Hebroni, nammangira Yehova kumeneko guwa la nsembe.


Ndipo Abrahamu anatambasula dzanja lake, natenga mpeni kuti amuphe mwana wake.


Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.


Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.


Ndipo anakonza nkhunizo, naduladula ng'ombe, naiika pankhuni. Nati, Dzazani madzi mbiya zinai, muwathire pa nsembe yopsereza ndi pankhuni.


Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.


ndipo anammanga Iye, namuka naye, nampereka Iye kwa Pilato kazembeyo.


Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.


Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegule pakamwa pake.


Khristu anatiombola ku temberero la chilamulo, atakhala temberero m'malo mwathu; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo.


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.


Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe?


amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa