Genesis 20:17 - Buku Lopatulika17 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Motero Abrahamu adapempherera Abimeleki, ndipo Mulungu adamchiza. Adachizanso mkazi wake pamodzi ndi antchito ake aakazi, kuti onsewo azitha kubala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Tsono Abrahamu anapemphera kwa Mulungu ndipo Mulunguyo anachiritsa Abimeleki, mkazi wake pamodzi ndi adzakazi ake kuti athenso kubereka ana. Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.