Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 20:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo panali pamene Mulungu anandiyendetsa ine kunyumba kwa atate wanga, ndinati kwa mkaziyo, Ichi ndicho chokoma mtima udzandichitire ine, konse kumene tidzafika ife, uzinena za ine, Iye ndiye mlongo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Motero pamene Mulungu adandituma kuchokera kunyumba kwa bambo wanga, kuti ndipite ku maiko achilendo, ndidaamuuza mkazi wangayu kuti, ‘Undiwonetse kuti ndiwedi wokhulupirika kwa ine, pouza aliyense kuti ndine mlongo wako, kulikonse kumene tizipita.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ndiye pamene Mulungu anati ndichoke ku nyumba ya abambo anga, ndinawuza mkazi wangayu kuti, ‘Kuti uwonetse kuti ndiwe mkazi wokoma mtima, uziwuza anthu kulikonse kumene tingapite kuti ndine mlongo wako.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 20:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Abramu, Tuluka iwe m'dziko lako, ndi kwa abale ako, ndi kunyumba ya atate wako, kunka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe;


Ndipo Abramu anayenda ulendo wake, nayendayenda kunka kumwera.


Koma ndiye mlongo wanga ndithu, mwana wa atate wanga, koma si mwana wa amai wanga: ndipo anakhala ndi ine mkazi wanga.


Kodi iye sanati kwa ine, Ndiye mlongo wanga: ndipo mkazi iye yekha anati, Iye ndiye mlongo wanga: ndi mtima wanga wangwiro ndi manja anga osachimwa ndachita ine ichi.


Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani?


Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.


Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poitanidwa, anamvera kutuluka kunka kumalo amene adzalandira ngati cholowa; ndipo anatuluka wosadziwa kumene akamukako.


Saulo nati, Mudalitsike inu kwa Yehova; chifukwa munandichitira ine chifundo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa