Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 19:35 - Buku Lopatulika

35 Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

35 Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

35 Motero usiku umenewo adamledzeretsanso, ndipo mwana wamng'onoyo adagona ndi bambo wake. Nthaŵi imeneyinso nkuti bamboyo ataledzera, kotero kuti sadadziŵe zochitikazo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

35 Choncho analedzeranso vinyo abambo awo usiku umenewonso, ndipo mwana wamkazi wamngʼono anapita nagona nawo. Abambo awo sanadziwenso kanthu pamene mwanayo anagona naye kapena pamene anadzuka.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 19:35
8 Mawu Ofanana  

Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.


Ndipo ana aakazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.


munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?


Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.


ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa