Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 17:5 - Buku Lopatulika

5 Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Sudzatchedwanso dzina lako Abramu, koma dzina lako lidzakhala Abrahamu; chifukwa kuti ndakuyesa iwe atate wa khamu la mitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Dzina lako silidzakhalanso Abramu, koma Abrahamu. Limeneli ndilo dzina lako, chifukwa ndikukusandutsa kholo la anthu a mitundu yambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Sudzatchedwanso Abramu; dzina lako lidzakhala Abrahamu, chifukwa ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri ya anthu.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 17:5
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Koma Sarai mkazi wako, usamutcha dzina lake Sarai, koma dzina lake ndi Sara.


Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.


Yakobo ndipo anafunsa iye, nati, Undiuze ine dzina lako. Ndipo iye anati, Undifunsa dzina chifukwa ninji? Ndipo anamdalitsa iye pamenepo.


Ndipo Mulungu anati kwa iye, Dzina lako ndi Yakobo; dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma dzina lako lidzakhala Israele: ndipo anamutcha dzina lake Israele.


natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova.


Abramu, (ndiye Abrahamu).


Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumtulutsa mu Uri wa kwa Akaldeya, ndi kumutcha dzina lake Abrahamu;


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


Ndipo panali m'mawa mwake, kuti Pasuri anatulutsa Yeremiya m'matangadzamo. Ndipo Yeremiya anati kwa iye, Yehova sanatche dzina lako Pasuri, koma Magorimisabibu.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.


Anadza naye kwa Yesu. M'mene anamyang'ana iye, anati, Uli Simoni mwana wa Yohane; udzatchedwa Kefa (ndiko kusandulika Petro).


monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa