Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 16:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo iye adzakhala munthu wa m'thengo; ndipo dzanja lake lidzakhala lotsutsana ndi anthu onse, ndi manja a anthu onse adzakhala otsutsana naye: ndipo iye adzakhala pamaso pa abale ake onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma mwana wako adzakhala ndi mtima wa chilombo, adzadana ndi aliyense, ndipo anthu onse adzadana naye. Adzakhala akudana ndi abale ake onse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 16:12
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'chipululu, nakhala wauta.


Ndipo anakhala iwo kuyambira ku Havila kufikira ku Suri, ndiko kum'mawa kwake kwa Ejipito, pakunka ku Asiriya: ndipo iye anakhala pamaso pa abale ake onse.


Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.


Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


Koma munthu wopanda pake asowa nzeru, ngakhale munthu abadwa ngati mwanawabulu.


Taonani, ngati mbidzi za m'chipululu atulukira kuntchito zao, nalawirira nkufuna chakudya; chipululu chiwaonetsera chakudya cha ana ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa