Ezara 4:3 - Buku Lopatulika3 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Koma Zerubabele, Yesuwa, ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a m'dziko la Israele adaŵayankha kuti, “Sitikusoŵa chithandizo chanu pa ntchito iyi yomangira Nyumba Mulungu wathu. Koma ife tokha tidzammangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi, mfumu ya ku Persiya, adatilamula.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.” Onani mutuwo |
Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.