Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 34:29 - Buku Lopatulika

29 Ndipo kunali pakutsika Mose paphiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

29 Ndipo kunali pakutsika Mose pa phiri la Sinai, ndi magome awiri a mboni m'dzanja lake la Mose, pakutsika iye m'phirimo, Mose sanadziwe kuti khungu la nkhope yake linanyezimira popeza Iye adalankhula naye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

29 Pamene Mose adatsika phiri la Sinai atanyamula miyala iŵiri yaumboni ija, sadadziŵe kuti nkhope yake njoŵala chifukwa cholankhula ndi Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

29 Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 34:29
22 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.


Ndipo atatha Iye kulankhula ndi Mose, paphiri la Sinai, anampatsa magome awiri a mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.


Ndipo Mose anatembenuka, natsika m'phirimo, magome awiri a mboni ali m'dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.


Ndipo ana a Israele anaona nkhope ya Mose, kuti khungu la nkhope ya Mose linanyezimira; ndipo Mose anaikanso chophimba pankhope pake, kufikira akalowa kulankhula ndi Iye.


Ndani akunga wanzeru? Ndani adziwa tanthauzo la mau? Nzeru ya munthu iwalitsa nkhope yake, kuduwa kwa nkhope yake ndi kusanduka.


ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.


Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye.


Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu.


Ndipo Iye anati kwa iwo, Kuli bwanji kuti munalikundifunafuna Ine? Simunadziwa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m'zake za Atate wanga?


Ndipo m'kupemphera kwake, maonekedwe a nkhope yake anasandulika, ndi chovala chake chinayera ndi kunyezimira.


Koma wochiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani; pakuti Yesu anachoka kachetechete, popeza panali anthu aunyinji m'malo muja.


Ndipo anatuluka, namtsata; ndipo sanadziwe kuti nchoona chochitidwa ndi mngelo, koma anayesa kuti alikuona masomphenya.


Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa;


Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine.


Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwe uko afuma;


Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mzinda kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mzinda.


Ndipo m'dzanja lake lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwiri; ndi m'kamwa mwake mudatuluka lupanga lakuthwa konsekonse; ndipo nkhope yake ngati dzuwa lowala mu mphamvu yake.


Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;


Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa