Eksodo 33:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Uchokeko kuno pamodzi ndi anthu amene udabwera nawo kuchokera ku Ejipito, ndipo upite ku dziko limene ndidalonjeza kuti ndidzapatsa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Pa nthaŵi imeneyo ndidaŵauza iwowo kuti, ‘Dziko limeneli ndidzalipatsa kwa zidzukulu zanu.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Onani mutuwo |