Eksodo 32:18 - Buku Lopatulika18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa ogonjetsa, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa olakika, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang'ombe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Koma Mose adati, “Phokoso limenelo silikumveka ngati phokoso la opambana pa nkhondo, kapenanso kulira kwa ogonjetsedwa. Ndikumva phokoso la kuimba.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Mose anayankha kuti, “Phokoso limeneli sindikulimva ngati phokoso la opambana nkhondo, kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.” Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.