Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:25 - Buku Lopatulika

25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osakanizika monga mwa machitidwe a wosakaniza; akhale mafuta odzoza opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osanganizika monga mwa machitidwe a wosanganiza; akhale mafuta odzoza opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 Tsono zonsezi udzapangire mafuta odzozera. Udzaziphatikize pamodzi monga momwe amachitira munthu wopanga zonunkhira. Mafuta amenewo adzakhale mafuta oyera, odzozera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:25
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Ndi ana ena a ansembe anasakaniza chisakanizo cha zonunkhira.


Ndiko ngati mafuta a mtengo wake pamutu, akutsikira kundevu, inde kundevu za Aroni; akutsikira kumkawo wa zovala zake.


Ndapeza Davide mtumiki wanga; ndamdzoza mafuta anga oyera.


Ndipo uveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ake omwe; ndi kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andichitire Ine ntchito ya nsembe.


Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.


Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.


ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;


Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.


ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;


ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi mphiko zake, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pakhomo, pa khomo la chihema;


Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.


Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao chihema, ndi zonse zili m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zake zonse; ndipo adzakhala wopatulika.


Ntchentche zakufa zinunkhitsa moipa ndipo zioletsa mafuta onunkhira a sing'anga; chomwecho kupusa kwapang'ono kuipitsa iye amene atchuka chifukwa cha nzeru ndi ulemu.


Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza chihema, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula.


Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;


ndipo msonkhano umlanditse wakupha munthu m'dzanja la wolipsa mwazi, ndi msonkhanowo umbwezere kumzinda wake wopulumukirako, kumene adathawirako; ndipo azikhalamo kufikira atafa mkulu wa ansembe wodzozedwa ndi mafuta opatulika.


Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa; mwa ichi Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wakudzozani ndi mafuta a chikondwerero chenicheni koposa anzanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa