Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 30:23 - Buku Lopatulika

23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka, mure woyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 “Utenge zonunkhira bwino kwambiri zokwanira makilogaramu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogaramu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa kinamoni, makilogaramu atatu a nzimbe zonunkhira bwino,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 “Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri,

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 30:23
20 Mawu Ofanana  

Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.


Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo zilizonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi lubani, ndi zonunkhira.


Ndi ana ena a ansembe anasakaniza chisakanizo cha zonunkhira.


Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya; m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.


mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma;


Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,


ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;


ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha zonunkhira zokoma za malo opatulika; azichita monga mwa zonse ndakuuza iwe.


ndi zonunkhira, ndi mafuta akuunikira, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza za fungo lokoma.


Anapanganso mafuta opatulika akudzoza nao, ndi chofukiza choona cha fungo lokoma, mwa machitidwe a wosakaniza.


ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhira a mure ndi chisiyo ndi sinamoni.


Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la mure, logona pakati pa mawere anga.


Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.


Narido ndi chikasu, nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani; mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.


Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndalama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi machimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.


Lubani andifumiranji ku Sheba, ndi nzimbe ku dziko lakutali? Nsembe zopsereza zanu sizindisekeretsa, nsembe zophera zanu sizindikondweretsa Ine.


Vedani ndi Yavani anagula malonda ako ndi thonje, unagulana nao chitsulo chosalala, ngaho, ndi nzimbe.


Amalonda a ku Sheba ndi a ku Raama anagulana nawe malonda; anagula malonda ako ndi zonunkhira zoposa zilizonse, ndi miyala iliyonse ya mtengo wake, ndi golide.


Ndipo zoyang'anira Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, ndizo mafuta a nyaliyo, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsembe yaufa kosalekeza, ndi mafuta odzoza, udikiro wa chihema chonse, ndi zonse zili m'mwemo, malo opatulika, ndi zipangizo zake.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa