Eksodo 30:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Aroni azidzachita mwambo wopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Ndi magazi a nyama zija za nsembe zopepesera machimo azidzayeretsera guwa limeneli kamodzi pa chaka. Zimenezi zizidzachitikanso m'mibadwo yanu yonse. Guwa limeneli lidzakhala loyera kwambiri, lopatulikira Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.” Onani mutuwo |