Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:36 - Buku Lopatulika

36 Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Nukonze ng'ombe yamphongo, ndiyo nsembe yauchimo yakuteteza nayo, tsiku ndi tsiku; ndipo uyeretsa guwa la nsembe, pakuchita choteteza pamenepo; ndipo ulidzoze kulipatula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Tsiku ndi tsiku uzipereka ng'ombe yamphongo yopepesera machimo, kuti machimowo akhululukidwe. Uyeretse guwalo pakuliperekera nsembe yopepesera machimo. Kenaka ulidzoze kuti likhale lopatulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:36
14 Mawu Ofanana  

Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni,


Nutengeko mwazi wake, ndi kupaka pa nyanga zinai za guwa, ndi pangodya zinai za phaka, ndi pa mkuzi wake pozungulira; motero uliyeretse ndi kulichitira chotetezera.


Masiku asanu ndi awiri uzikonzera mbuzi tsiku ndi tsiku, ikhale nsembe yauchimo; akonzerenso mwanawang'ombe, ndi nkhosa yamphongo ya zoweta zopanda chilema.


Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika paguwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.


Koma ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndi mbuzi ya nsembe yauchimo, zimene mwazi wao analowa nao kuchita nao chotetezera m'malo opatulika, atuluke nazo kunja kwa chigono; natenthe ndi moto zikopa zao, ndi nyama zao, ndi chipwidza chao.


Ndipo kunali kuti tsiku lomwe Mose anatsiriza kuutsa chihema, nachidzoza ndi kuchipatula, ndi zipangizo zake zonse, ndi guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, nazidzoza ndi kuzipatula;


Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizingathe konse kuchotsa machimo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa