Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 29:30 - Buku Lopatulika

30 mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Mwana wa Aroni womloŵera m'malo kuti akhale wansembe, azidzavala zimenezi masiku asanu ndi aŵiri, pamene akuloŵa m'chihema chamsonkhano kukatumikira m'malo oyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 29:30
17 Mawu Ofanana  

Ndipo analinda masiku ena asanu ndi awiri; natulutsanso njiwayo m'chingalawamo;


Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabwerenso konse kwa iye.


Masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa; lingakhale tsiku loyamba muzichotsa chotupitsa m'nyumba zanu; pakuti aliyense wakudya mkate wa chotupitsa kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzachotsedwa kwa Israele.


Ndipo zovala zopatulika za Aroni zikhale za ana ake aamuna pambuyo pake, kuti awadzoze atazivala, nadzaze manja ao atazivala;


Ndipo utenge nkhosa yamphongo yodzaza manja, nuphike nyama yake m'malo opatulika.


Ndipo utero nao Aroni, ndi ana ake aamuna, monga mwa zonse ndakuuza; udzaze manja ao masiku asanu ndi awiri.


Masiku asanu ndi awiri achite chotetezera guwali ndi kuliyeretsa, momwemo alipatule.


ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirire pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;


Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lake achite ntchito ya nsembe m'malo mwa atate wake, achite chotetezera, atavala zovala zabafuta, zovala zopatulikazo.


Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake aamuna, ndi akulu a Israele;


Pamenepo Aroni anasendera kufupi kwa guwa la nsembe, napha mwanawang'ombe wa nsembe yauchimo, ndiyo ya kwa iye yekha.


Ndipo Mose anavula Aroni zovala zake, naveka Eleazara mwana wake; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba paphiri. Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa