Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo azivale Aroni ndi ana ake, pakulowa iwo ku chihema chokomanako, kapena poyandikiza iwo kuguwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zake pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Aroni ndi ana ake azivala zimenezi nthaŵi zonse akamapita ku chihema chamsonkhano kapena ku guwa, kukanditumikira ku malo opatulika aja, kuwopa kuti angachimwe ndipo angafe. Lamulo limeneli, lonena za Aroni ndi zidzukulu zake, ndi lokhazikika mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Aaroni ndi ana ake ayenera kuvala akabudulawo pamene akulowa mu tenti ya msonkhano kapena pamene akupita ku guwa lansembe kukatumikira malo oyera kuopa kuti angachimwe ndi kufa. “Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aaroni ndi zidzukulu zake.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:43
18 Mawu Ofanana  

Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angaoneke maliseche ako pamenepo.


Aroni ndi ana ake aikonze m'chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kunja kwa nsalu yotchinga yokhala kumboni, kuyambira madzulo kufikira m'mawa; likhale lemba losatha mwa mibadwo yao, alisunge ana a Israele.


asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.


Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam'kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi mu Kachisi.


naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.


Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.


Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova;


Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.


Likhale lemba losatha m'mibadwo yanu m'nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.


Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;


Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.


Kunena za khamu, pakhale lemba limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo wakukhala kwanu, ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; monga mukhala inu, momwemo mlendo pamaso pa Yehova.


Ndipo kuyambira tsopano ana a Israele asayandikize chihema chokomanako, angamasenze uchimo kuti angafe.


Ndipo simudzasenzapo uchimo, mutakwezako zokometsetsa zake; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israele, kuti mungafe.


Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israele; chifukwa cha kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna, likhale lemba losatha.


Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kuchita Paska, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wake; popeza sanabwere nacho chopereka cha Yehova pa nyengo yake yoikidwa, munthuyu asenze kuchimwa kwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa