Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 28:42 - Buku Lopatulika

42 Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche ao; ziyambire m'chuuno zifikire kuntchafu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

42 Uwasokerenso zovala za miyendo za bafuta wa thonje losansitsa kubisa maliseche ao; ziyambire m'chuuno zifikire kuntchafu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

42 Uŵasokere akabudula ofika m'ntchafu, kuti asamaonetse maliseche.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

42 “Uwapangire akabudula a nsalu yofewa oyambira mʼchiwuno kulekeza mʼntchafu kuti asamaonetse maliseche.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 28:42
8 Mawu Ofanana  

Kapena usakwere ndi makwerero ku guwa langa la nsembe, kuti angaoneke maliseche ako pamenepo.


ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,


Ndipo kudzatero, polowa iwo kuzipata za bwalo lam'kati avale zovala zabafuta; koma zaubweya asazivale ponditumikira Ine m'zipata za bwalo la m'kati, ndi mu Kachisi.


Akhale nao akapa abafuta pamitu pao, ndi akabudula m'chuuno mwao; asavale m'chuuno kanthu kalikonse kakuchititsa thukuta.


Avale malaya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zovala za kumiyendo pathupi pake, nadzimangire m'chuuno ndi mpango wabafuta, navale nduwira yabafuta; izi ndi zovala zopatulika; potero asambe thupi lake ndi madzi, ndi kuvala izi.


Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.


kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;


ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa