Eksodo 28:30 - Buku Lopatulika30 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201430 Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa chapachifuwa cha chiweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula chiweruzo cha ana a Israele pamtima pake pamaso pa Yehova kosalekeza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa30 M'chovala chapachifuwacho uziikamo zinthu zoyera za Chauta zotchedwa Urimu ndi Tumimu, kuti zimenezo zikhale pa chifuwa cha Aroni akamapita kwa Chauta. Motero Aroni akakhala pamaso pa Chauta, nthaŵi zonse adzakhala ndi zomthandiza kuweruza bwino mpingo wa Israele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero30 Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova. Onani mutuwo |