Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 25:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 “Upange ndi golide wabwino kwambiri chivundikiro cha bokosi, kutalika kwake masentimita 114, kupingasa kwake masentimita 69.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 25:17
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo Davide anapatsa Solomoni mwana wake chifaniziro cha chipinda cholowera cha Kachisi, ndi cha nyumba zake, ndi cha zosungiramo chuma zake, ndi cha zipinda zosanjikizana zake, ndi cha zipinda zake za m'katimo, ndi cha Kachisi wotetezerepo;


Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.


Ndipo uziika chotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulika kwambiri.


likasa, ndi mphiko zake, chotetezerapo, ndi nsalu yotchinga yotseka;


Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.


Ndipo anatenga mboniyo, naiika m'likasa, napisa mphiko palikasa, naika chotetezerapo pamwamba pa likasa;


Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali paphiri lopatulika la Mulungu, anayendayenda pakati pa miyala yamoto.


amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitingathe kunena tsopano paderapadera.


ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa