Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:26 - Buku Lopatulika

26 Munthu akampanda mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu chifukwa cha diso lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Munthu akampanda mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, padiso, nalithudzula, azimlola amuke waufulu chifukwa cha diso lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 “Munthu akamenya kapolo wamwamuna kapena wamkazi pa diso, nkulikoloola disolo, ammasule kapoloyo, kuti akhale mfulu chifukwa cha disolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 “Ngati munthu amenya wantchito wake wa mwamuna kapena mdzakazi wake pa diso ndi kuliwononga, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a diso lake.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:26
14 Mawu Ofanana  

Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu aakazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.


Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.


kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.


Pakuti Iye wofuna chamwazi awakumbukira; saiwala kulira kwa ozunzika.


Munthu akakantha mnyamata wake, kapena mdzakazi wake, ndi ndodo, ndipo akafa padzanja pake; ameneyo alangidwe ndithu.


diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi,


kutentha kulipa kutentha, bala kulipa bala, mkwapulo kulipa mkwapulo.


Ndipo akagulula dzino la mnyamata wake, kapena dzino la mdzakazi wake, azimlola amuke waufulu chifukwa cha dzino lake.


Ndipo, ambuye, inu, muwachitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali mu Mwamba, ndipo palibe tsankho kwa Iye.


Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.


Ambuye inu, chitirani akapolo anu cholungama ndi cholingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye mu Mwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa