Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:32 - Buku Lopatulika

32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Tsono Mose adati, “Chauta walamula kuti ‘Musungeko mana ena kuti zidzukulu zanu zidzaone chakudya chimene ndidakupatsani m'chipululu, nditakutulutsani ku Ejipito kuja.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:32
11 Mawu Ofanana  

Kumbukirani zodabwitsa zake adazichita; zizindikiro zake ndi maweruzo a pakamwa pake;


Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.


Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mphika, nuthiremo mana odzala omeri, nuuike pamaso pa Yehova, usungikire mibadwo yanu.


koma chinthu ichi ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti chikukomereni.


Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za chikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira chakudya.


Ndipo m'mene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.


Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.


okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaaphukayo, ndi magome a chipangano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa