Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo atakamuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo atasansuka mame adagwawo, taonani, pankhope pa chipululu pali kanthu kakang'ono kamphumphu, kakang'ono ngati chipale panthaka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Mamewo atangokamuka, panthakapo m'chipululu muja padapezeka tinthu tina topyapyala, tambee ngati chipale, ndiponso tonyata.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:14
7 Mawu Ofanana  

ndi mkate wochokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi otuluka m'thanthwe munawatulutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.


Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.


Apatsa chipale chofewa ngati ubweya; awaza chisanu ngati phulusa.


Ndipo anawavumbitsira mana, adye, nawapatsa tirigu wa kumwamba.


Ndipo mbumba ya Israele inautcha dzina lake Mana; ndiwo ngati zipatso zampasa, oyera; powalawa akunga timitanda tosakaniza ndi uchi.


Ndipo anakuchepetsani, nakumvetsani njala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwe, angakhale makolo anu sanawadziwe; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka m'kamwa mwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa