Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 16:12 - Buku Lopatulika

12 Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndamva madandaulo a ana a Israele; lankhula nao ndi kuti, Madzulo mudzadya nyama, ndi m'mawa mudzakhuta mkate; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Ndamva madandaulo a Aisraele. Ndiye uŵauze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama, ndipo m'maŵa mudzadya buledi, choncho mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 16:12
17 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu uja wa Mulungu anafikako, nalankhula ndi mfumu ya Israele, nati, Atero Yehova, Popeza Aaramu amati, Yehova ndiye Mulungu wa kumapiri, osati Mulungu wa kuzigwa, mwa ichi ndidzapereka unyinji uwu waukulu m'dzanja mwako, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.


Anafunsa ndipo Iye anadzetsa zinziri, nawakhutitsa mkate wakumwamba.


Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,


kuti akhulupirire kuti wakuonekera Yehova Mulungu wa makolo ao, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo.


ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aejipito.


Atero Yehova, Ndi ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova; taonani, ndidzapanda madzi ali m'mtsinje ndi ndodo ili m'dzanja langa, ndipo adzasanduka mwazi.


Ndipo Yuda ndi mizinda yake yonse adzakhalamo pamodzi; alimi, ndi okusa zoweta.


Ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wao ndili nao, ndi kuti iwo, nyumba ya Israele, ndiwo anthu anga, ati Ambuye Yehova.


Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.


Ndipo nyumba ya Israele idzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, kuyambira tsiku ilo ndi m'tsogolomo.


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu; potero dzipatuleni, ndipo muzikhala oyera; pakuti Ine ndine woyera; ndipo musamadziipsa ndi chokwawa chilichonse chakukwawa pansi.


Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.


Ndipo anthu osokonezeka ali pakati pao anagwidwa nacho chilakolako; ndi ana a Israele omwe analiranso, nati, Adzatipatsa nyama ndani?


Ndileke khamu loipa ili lakudandaula pa Ine kufikira liti? Ndidamva madandaulo a ana a Israele, amene amandidandaulira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa