Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:32 - Buku Lopatulika

32 Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Muka nazoni zoweta zanu zazing'ono ndi zazikulu, monga mwanena; chokani, ndi kundidalitsa inenso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Mutenge nkhosa zanu, mbuzi zanu ndi ng'ombe zanu zomwe, monga momwe mudanenera, ndipo muchoke. Mukapemphere kuti nanenso andidalitseko.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:32
8 Mawu Ofanana  

ndiponso mtunduwo adzautumikira, Ine ndidzauweruza: ndiponso pambuyo pake adzatuluka ndi chuma chambiri.


Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.


Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.


kuti apereke nsembe zonunkhira bwino kwa Mulungu wa Kumwamba, napempherere moyo wa mfumu ndi wa ana ake.


Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.


Ndipo Mose anati, Tidzamuka ndi ana athu ndi akulu athu, ndi ana athu aamuna ndi aakazi; tidzamuka nazo nkhosa zathu ndi ng'ombe zathu; pakuti tili nao madyerero a Yehova.


Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.


Pembani kwa Yehova; chifukwa akwanira ndithu mabingu a Mulungu ndi matalala; ndipo ndidzakulolani mumuke, osakhalanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa