Danieli 7:11 - Buku Lopatulika11 Pamenepo ndinapenyera chifukwa cha phokoso la mau aakulu idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adachipha chilombochi, ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Pamenepo ndinapenyera chifukwa cha phokoso la mau akulu idanena nyangayi; ndinapenyera mpaka adachipha chilombochi, ndi kuononga mtembo wake, ndi kuupereka utenthedwe ndi moto. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.