Danieli 6:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo podziwa Daniele kuti adatsimikiza cholembedwacho, analowa m'nyumba mwake, m'chipinda mwake, chimene mazenera ake anatseguka oloza ku Yerusalemu; ndipo anagwada maondo ake tsiku limodzi katatu, napemphera, navomereza pamaso pa Mulungu wake monga umo amachitira kale lonse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. Onani mutuwo |