Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:43 - Buku Lopatulika

43 Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Ndipo adzachita mwamphamvu ndi chuma cha golide, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Ejipito; Libiya ndi Akusi adzatsata mapazi ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:43
9 Mawu Ofanana  

Anakwera ndi magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kutuluka mu Ejipito ngosawerengeka, Alibiya, Asuki, ndi Akusi.


Ndipo anyamata ako onse awa adzanditsikira, nadzandigwadira, ndi kuti, Tulukani inu, ndi anthu onse akukutsatani; ndipo pambuyo pake ndidzatuluka. Ndipo anatuluka kwa Farao wakupsa mtima.


Persiya, Kusi, ndi Puti pamodzi nao, onsewo ndi chikopa ndi chisoti chachitsulo;


Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka.


Koma mbiri yochokera kum'mawa ndi kumpoto idzamvuta; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuononga konse ambiri.


Kusi ndi Ejipito ndiwo mphamvu yake, ndiyo yosatha, Puti ndi Libiya ndiwo akukuthandiza.


Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa