Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:41 - Buku Lopatulika

41 Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:41
9 Mawu Ofanana  

Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.


Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.


Ejipito, ndi Yuda, ndi Edomu, ndi ana a Amoni, ndi a Mowabu, ndi onse ometa m'mphepete mwa tsitsi lao, okhala m'chipululu; pakuti amitundu onse ali osadulidwa, ndi nyumba ya Israele ili yosadulidwa m'mtima.


Koma iye amene amdzera kulimbana naye adzachita chifuniro chake cha iye mwini; palibe wakulimbika pamaso pake; ndipo adzaima m'dziko lokometsetsalo, ndi m'dzanja mwake mudzakhala chionongeko.


Adzatambalitsiranso dzanja lake kumaiko; dziko la Ejipito lomwe silidzapulumuka.


Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza.


Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing'ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwera, ndi kum'mawa, ndi kudziko lokometsetsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa