Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Danieli 11:41 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

41 Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lake ndi awa: Edomu, ndi Mowabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:41
9 Mawu Ofanana  

“Komabe masiku akutsogolo ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,” akutero Yehova. Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.


“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,” akutero Yehova.


Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”


Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija.


Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka.


Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”


Pa imodzi mwa nyangazo panatuluka nyanga imene inali yocheperapo koma inakula kwambiri kuloza kummwera ndi kummawa ndi kuloza dziko lokongola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa