Danieli 11:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzapambana. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo atauchotsa unyinjiwo udzakwezeka mtima wake; ndipo adzagwetsa zikwi makumimakumi, koma sadzalakika. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Gulu la nkhondoli likadzagwidwa, mfumu yakummwera idzayamba kudzikuza ndipo idzapha anthu miyandamiyanda, koma kupambanaku sikudzapitirira. Onani mutuwo |
koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; ndipo anabwera nazo zotengera za nyumba yake kwa inu; ndi inu ndi akulu anu, akazi anu ndi akazi anu aang'ono, mwamweramo vinyo; mwalemekezanso milungu yasiliva, ndi yagolide, yamkuwa, yachitsulo, yamtengo, ndi yamwala, imene siiona kapena kumva, kapena kudziwa; ndi Mulungu amene m'dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitire ulemu.