Amosi 7:1 - Buku Lopatulika1 Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu wa chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawusengera mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa udzu a chibwereza; ndipo taonani, ndicho chibwereza atawasengera mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Izi ndizo zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Chauta ankapanga dzombe pa nthaŵi yoti mfumu inali itamweta kale udzu, ndipo udzuwo unkaphukanso kachiŵiri. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. Onani mutuwo |
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.