Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 6:4 - Buku Lopatulika

4 ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi oŵakongoletsa ndi minyanga yanjovu, inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu, nkumachita phwando la nyama ya anaankhosa osakhwima ndi ya anaang'ombe onenepa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu, mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu. Mumadya ana ankhosa onona ndi ana angʼombe onenepa.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 6:4
18 Mawu Ofanana  

Ndipo iwo anakhala pansi kuti adye chakudya; ndipo anatukula maso ao, nayang'ana, ndipo taonani, ulendo wa Aismaele anachokera ku Giliyadi ndi ngamira zao, zilinkunyamula zonunkhira ndi mafuta amankhwala ndi mure alinkumuka kutsikira nazo ku Ejipito.


panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.


Kunenepa kwao kutuzulitsa maso ao, malingaliro a mitima yao asefukira.


koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa.


Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino.


Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.


Taona, mphulupulu ya mng'ono wako Sodomu ndi iye, kudzikuza, kuchuluka kwa chakudya, ndi kupumula kwa mtambasali, anali nako iye ndi ana ake; ndipo sanalimbitse dzanja la wosauka ndi wosowa.


ndipo unakhala pa kama waulemu, pali gome lokonzekeratu patsogolo pake; pamenepo unaika chofukiza chonga ndi mafuta anga.


Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.


Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.


Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.


Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;


Mwadyerera padziko, ndipo mwachita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa