Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 5:6 - Buku Lopatulika

6 Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima mu Betele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Betele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Muchite zimene Chauta afuna, kuti mukhalebe ndi moyo. Mukapanda kutero, adzatentha banja la Yosefe ngati moto, ndipo motowo udzapsereza a ku Betele popanda wina wouzimitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 5:6
28 Mawu Ofanana  

Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinachimwa; chifukwa chake, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.


Ndipo munthu ameneyo Yerobowamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomoni anamuona mnyamatayo kuti ngwachangu, anamuika akhale woyang'anira wa ntchito yonse ya nyumba ya Yosefe.


chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.


Pamene munati, Funani nkhope yanga; mtima wanga unati kwa Inu. Nkhope yanu, Yehova, ndidzaifuna.


Pakuti Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am'ndende ake.


Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.


Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;


Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.


Mudzidulire nokha kwa Yehova, chotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala mu Yerusalemu; ukali wanga ungatuluke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe anu.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


nuziti kwa dziko la Israele, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'chimake, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.


Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?


Unene nao, Atero Ambuye Yehova, Taonani, ndidzatenga mtengo wa Yosefe uli m'dzanja la Efuremu, ndi wa mafuko a Israele anzake, ndi kuwaika pamodzi ndi mtengo wa Yuda, ndi kuiyesa mtengo umodzi; ndipo idzakhala umodzi m'dzanja langa.


Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.


Funani chokoma, si choipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wa makamu adzakhala ndi inu, monga munena.


Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israele, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;


akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.


Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m'dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.


Ndipo ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda, ndi kusunga nyumba ya Yosefe, ndipo ndidzawakhalitsa, pakuti ndawachitira chifundo; ndipo adzakhala monga ngati sindinawataye konse; pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, ndipo ndidzawamvera.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye moto wonyeketsa, ndi Mulungu wansanje.


Ndipo adzaligawa magawo asanu ndi awiri; Yuda adzakhala m'malire ake kumwera, ndi a m'nyumba ya Yosefe adzakhala m'malire mwao kumpoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa