Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Akolose 2:22 - Buku Lopatulika

22 (ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 (ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe.

Onani mutuwo Koperani




Akolose 2:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Ndipo tsiku limenelo gonthi adzamva mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona potuluka m'zoziya ndi mumdima.


Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, kapena chokhumba akazi, kapena kusamalira milungu iliyonse; pakuti idzadzikuza koposa onse.


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;


usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,


osasamala nthano zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho choonadi.


Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,


Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mzinda waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa