Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ambuye athu, amene mauŵa akunena za Iwo, anali a fuko lina. Ndipo palibiretu wa fuko limeneli amene adatumikirapo ku guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:13
6 Mawu Ofanana  

chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.


Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.


Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?


Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.


Pakuti kwadziwikadi kuti Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhule kanthu ka ansembe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa