Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 7:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo pakadakhala ungwiro mwa unsembe wa Chilevi (pakuti momwemo anthu analandira chilamulo), pakadatsala kusowa kotani kuti auke wansembe wina monga mwa dongosolo la Melkizedeki, wosayesedwa monga mwa dongosolo la Aroni?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Malamulo amene Aisraele adalandira, anali okhazikika pa unsembe wa Levi. Tsono achikhala kudaali kotheka kukhala angwiro mwa unsembe umenewu, sikukadafunikanso unsembe wina, wonga uja wa Melkizedeki, wosiyana ndi wonga uja wa Aroni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni?

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 7:11
17 Mawu Ofanana  

Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.


Koteronso ife, pamene tinali akhanda, tinali akapolo akumvera miyambo ya dziko lapansi;


koma tsopano, podziwa Mulungu inu, koma makamaka podziwika ndi Mulungu, mubwereranso bwanji kutsata miyambo yofooka ndi yaumphawi, imene mufuna kubwerezanso kuichitira ukapolo?


wotchedwa ndi Mulungu mkulu wa ansembe monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


Monga anenanso mwina, Iwe ndiwe wansembe wa nthawi zonse monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


m'mene Yesu mtsogoleri analowamo chifukwa cha ife, atakhala mkulu wa ansembe nthawi yosatha monga mwa dongosolo la Melkizedeki.


pakuti pajapo anali m'chuuno cha atate wake, pamene Melkizedeki anakomana naye.


Pakuti posandulika unsembe, kufunikanso kuti lamulo lisandulike.


Pakuti Iye amene izi zineneka za Iye, akhala wa fuko lina, wa ili palibe munthu watumikira guwa la nsembe.


Ndipo kwadziwikatu koposa ndithu, ngati auka wansembe wina monga mwa mafanidwe a Melkizedeki,


koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).


Pakuti loyamba lija likadakhala lopanda chilema sakadafuna malo a lachiwirilo.


Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa